Chifundo Chikonga - Amayankha lyrics | LyricsFreak
Correct  |  Mail  |  Print  |  Vote

Amayankha Lyrics

Chifundo Chikonga – Amayankha Lyrics

Ho-yee mama wee! ah yeah
Ooh yeah aah mthefile
O! mama wee!

Anali kuti dzana, mtima utawawa
Nkhawa zitafika, anabwerera m'mbuyo
Analira kosatha, usiku ndi usana
Atasweka mtima m'vuto lawo
Anamuuza Yesu, atathedwa nzeru
Anayembekeza, amayankha
Anamuuza Yesu, atathedwa nzeru
Anayembekeza, amayankha

Chorus
Anamuuza Yesu (Amayankha)
Anayitanirabe (Amayankha)
Dzina la Yehova (Amayamkha)
Zonse zinasintha (Amayankha)

Amayankha... yeah ihh

Anali kuti dzana, litavuta banja
Atakhumudwitsidwa misonzi ikutsika
Anadera nkhawa ntchito itasowa
Anavomereza kuti sadzayipeza
Anamuuza Yesu, atathedwa nzeru
Anayembekeza poti amayankha
Anamuuza Yesu, atathedwa nzeru
Anayembekeza ena nkumadabwa

Chorus
Anamuuza Yesu (Amayankha)
Anayitanirabe (Amayankha)
Dzina la Yehova (Amayamkha)
Zonse zinasintha (Amayankha)

Amayankha ah oh Amayankha

Bridge

Nanga ukulira chani iwe?
Pukuta misonzi
Zabwino zidzera oh, iwo oyembekeza, ooh uohuh!

Chorus til end
Share lyrics
×

Amayankha comments